0
Skip to Content
ACTS
Home
About
ACTS Divinity
ACTS Ignite
International
Discipleship Resources
Apply
Donate
Student Portal
ACTS
Home
About
ACTS Divinity
ACTS Ignite
International
Discipleship Resources
Apply
Donate
Student Portal
Home
About
ACTS Divinity
ACTS Ignite
International
Discipleship Resources
Apply
Donate
Student Portal
  • Mulungu m’modzi Oona_utatu wa Mulungu- amene ndi wamuyaya wodalitsika muubwino wake onse ndi wodzala ndi chikondi, alipo yekha ndipo ndi wa mphamvu zonse. Sangagawidwe muziduswa komanso ali muumodzi mwa umulungu chidzalo Cha chiyero chonse chimene sichidaoneke pa dziko lapansi.

    Atate ndi Mulungu, Mwana ndi Mulungu ndinso Mzimu Woyela ndi Mulungu; koma si milungu itatu, koma Mulungu m’modzi mu utatu. Mu utatu Woyera umenewu palibe oposa nzake, palibe wamkulu palibe wang’ono. Onse atatu ndi amuyaya komanso ofanana. Siogawikana payekha payekha ndi Mulungu m’modzi ofanana, waulemu ndi mphamvu ndiye pa zonse utatu pa umodzi ndipo umodzi pa utatuwu ndi oyenera kupembedzedwa.

    Atate sadapangidwe kapena kulengedwa kapena kubalidwa ndi wina aliyense. Mwana sadapangidwe kapena kulengedwa koma adabadwitsidwa mwa Mulungu yekha. Mzimu Woyela sadapangidwe kapena kulengedwa kapena kubalidwa, koma ndiochokera mwa Atate ndi Mwana.

    Atate, Mwana ndi Mzimu Woyela ndi amodzi, sasiyana pa chimene ali ndi pachimene apanga, amapanga chiganizo chimodzi. Atatuwa ndi m’modzi mu chikhalidwe komanso muchimene iwo ali; oposa zonse, wamuyaya, osasitha, opezeka paliponse, odziwa zonse, wamphamvu zonse, wa nzeru zonse, woyera, wabwino ndi odzala ndi chifundo.

    Iye amadziwa kuchokera ku mapeto mpaka kumayambiriro a zinthu zonse, mu nzeru zake zakuya ndi chikondi utatu Woyera wa uMulungu  kuchokera kunthawi zosayamba wakhala akuitana anthu amitundu yonse ndi a malilime osiyanasiyana ku phwando lake, kuwalumikizitsa kwa Mwana wake mu chidzalo Cha Mzimu Woyera ngati chuma chake, ku chiyamiko cha ulemelero wa chisomo chake. Kotero mu utatu Woyera wa muyaya wa  umulungu, Atate Mwana adaikidwiratu maziko adziko la pansi asadaikidwe kudzakhala mpulumutsi kudzera mu kukhetsa mwazi, kuti tikathe kulandira chidzalo Cha moyo mwa iye ndi kulemekeza utatu wa  Umulungu monga Mfumu ya muyaya, yachikhalire, yosaoneka ndi maso, amene ndi wa nzeru mwa yekha ku nthawi zosatha. Amen (Numeri 6:22-27; Yesaya 6:3; Mateyu 3:16-17, 28:19; Yohane 15:26; 1 Yohane 5: 7)

  • Muchikondi chake chachikulu, Mulungu adalenga zonse kopanda kuchokera ndipo adati zilibwino. Cholengedwa chilichonse chimadalira Mulungu nthawi zonse pokhala iye otisakira zosowa zathu ndi kulamulira zinthu zonse. Iye Ali amwamba pa zonse ndipo zabwino zonse zimadalira ubwino wa Mulungu- wabwinoyu.

    Kotero tiyenera tigwade kwa Mulungu wa mphamvu zonseyi, amene payekha ndi wabwino, timasangalara mu ubwino wake umene watiitanira kuti tigawane naye limodzi ndi ubwino wake mu chilengedwe chake watiitana kuti tikachisamalire. Angakhale timagwadira iye mwa mantha iye samatipondereza ku mapazi ake. Mulungu m’modzi wabwinoyu adalenga anthu onse, mwamuna ndi mkazi, kuchokera mu chikondi chake ndi muchifanizo chake.

    Kulengedwa mwa Adamu, zitanthauza kuti tili olengedwa ofana mu chifanizo ndi muchikhalidwe Cha Mulungu. Kotero tiyenera kulemekeza ndi kutetezera umoyo wa munthu kuyambira pakutenga pakati kufikira imfa.

    Adalengedwa mwamuna ndi mkazi, anthu adadalitsidwa ndi Mlengi popeleka ukwati ngati mgwirizano oyera wa moyo onse pakati pa mwamuna m’modzi ndi mkazi m’modzi mu akukhala moona mtima kwa wina ndi nzake otsekukira ku madalitso a Mulungu oti akaberekane ndi kuchulukana. Banja ndi chinthu Cha ulemu wake, chomwe ndi chinsisi choyera. Kotero banja lionetsera chithunzithuzi cha chikondi Cha Khristu pa mpingo wake ndipo banja likuyenera kulemekezedwa ndi onse. Sionse amene adaitanidwira kukhala pa ukwati ndipo ambuye pakhani yakudzipaturira kwa Mulungu posakwatira ndipo malemba akuti ichinso ndi chinthu chabwino, izi zimaonetsera umoyo wa mtsogolo wa kuuka kwa akufa ndipo likuyenera kulemekezedwa ndi onse.

    Angakhale taona ubwino onsewu wa Mulungu mu chilengedwe chake, koma kuchokera mwa munthu m’modzi, Adamu (Tate wathu pa chilengedwe ndi Tate wa pangano) dziko lonse lidachimwa.  Monga momwe tidalengedwa tonse chifanizo Cha Mulungu, kotero kudzera mu kuchimwa kwa Adamu tidagawana uchimo ndi kusaweruzika. Palibe ochimwa kwambiri kapena ochimwa pang’ono, tonse tachimwa mwa Adamu.

    Tsopano, kudzera mu kugwa muuchimo kwa Adamu, chikhalidwe chonse Cha anthu (kupaturapo Ambuye wathu Yesu Khristu amene adabwera kudzatipulumutsa ku uchimo) chidavunda ndi uchimo umene wakhala ngati mbali imodzi ya ife. Chikhalidwe chovunda ichi ndi chomwe chikuonetsa kuti uchimo udazika mizu pakati panthu. Chikhalidwe chonse Cha munthu chidaonongeka kamba ka uchimo, mphamvu yonse ya chikhalidwe Cha munthu idasokonekera ndipo cholinga Cha Mulungu pa munthu zidaonongeka.  Kumvetetsa kwa munthu kudadetsedwa ndi umbuli, kuukira, kudzikonda. Kotero muchikhalidwe Cha umunthu palibe mphamvu Ina iliyonse ya payekha imene angathe kubwereranso pamaso pa Mulungu angakhale atachita ntchito zabwino.

    Njira yokhayo yomwe tingathe kumasuka ku uchimo ndiko kutembenuka kusiya uchimo ndi kuyang’ana kwa Khristu kudzera mu mphatso ya chisomo Cha kubadwanso mwatsopano. Kubadwanso mwatsopano ndi kusintha kwa uzimu kumene kumachitika m’moyo wa munthu kudzera mwa Mzimu Woyera pa kumva uthenga wabwino, umene umatidzutsa ku imfa ya uzimu kuchoka ku chibvundi kupita ku moyo watsopano mwa Khristu ndipo timakhala agwiri ntchito anzake.

    Akufunika kwa kulapa sikutheka pamene munthu watembenuka mtima koma moyo wake onse wa okhulupirira uyenera kukhala moyo wakulapa. Kuya kwa uchimo wathu kutanthauza kuti kulapa kuyenera kukuta madera onse a moyo wa okhulupirira.

     Kotero pamene tikura muchifanizo chake Cha Khristu mkatikati mwa moyo wathu wa chikhristu, tisaope kapena kuthawa kulapa. Tisamukane Mzimu Woyera pamene akutitsutsa pa moyo wathu, tiyeni tipemphere kuti maso athu apenye mlingo wa uchimo pa moyo wathu ndi kubwerera kwa mpulumutsi wathu.

    Kulapa uku sichimangokhala kokha chisomo kwa iwo amene adaukitsidwa kwatsopano mwa Khristu koma kuti kulapaku mkofunikira kwambiri pa moyo wathu wa chikhristu.

     Patsiku la chiweruzo osatembenuka mtima adzalalandira chilango kwa Mulungu woweruza wa chilungamo. Kukana kulapa sichizindikiro Cha chikhulupiriro choona mwa Khristu ayi koma chenjezo la chiweruzo chomwe chili mkudza. (Masalmo 51:5; Mateyu 25:41; Yohane 3:3; Machitidwe 2:38; 17:30Aroma 3:10-18; Aefeso 2:1-3; Yohane 5:19; Chbvumbulutso 20:12-15; 21:8.

  • Mulungu odzala mchisomo ndi chikondi adatumiza Mwana wake obadwa yekha kuno kudziko kutibweretsera chipulumutso. Ambuye wathu Yesu Khristu, amene ali mawu a muyaya, Mwana wa Atate adakakhala thupi mu mimba ya m’namwaliyo Mariya, navala chifanizo Cha munthu, kuti nthawi yomweyo ali limodzi ndi Atate, kuonetsera chikhalidwe chake monga Mulungu oona amene ali pakati pathu, kuonetsera chikhalidwe Cha umunthu pakati pathu monga Mulungu muthupi. Mwa Mwana wa munthu, ulemelero wa Mulungu osaonekayo umaonekera mwa iye, odzala ndi chifundo ndi choonadi. Sadataye chimene iye adali, koma kamba ka ife adzatenga maonekedwe athupi kuti mu umodzi wa iye, zikaoneke zomwe achita kuti ndi Mulungu -munthu.

    Kudzera m’moyo wake opanda uchimo, ambuye wathu Yesu Khristu adamvera lamuro la Mulungu ndipo adakwaniritsa chiyero chonse kwa ife. Ndipo podzipeleka yekha nsembe kwa Atate kudzera pa imfa ya pa mtanda, adakhetsa mwazi ndi kutifera kamba ka machimo athu, natenga chilango chathu. Khristu watiombola ife ku temberero la chilamuro potenga temberero pa ntchito yake ya kukondweretsa Mulungu ndi cholinga Cha kutitetezera ife ku imfa.

    Pa kuuka kwake kwa ulemelero, Yesu wachipambanoyu akupeleka moyo watsopano kwa anthu ake. Kuuka mwamkokomo m’manda pa tsiku lachitatu, atagonjetsa mphamvu ya tchimo, imfa, gehena ndi m’dierekezi, kuuka kwa Khristu kwakhala ndondomeko ndi lonjezo lathu lolozera za tsiku lachimaliziro, pamene adzatidzutsa ife m’matupi athu osandulikira ku ulemelero wake ‘kusainthika kwa thupi lathu kukhala la ulemelero’ (Afilipi 3:21)

    Osati kusandulikira zinthu zopanda pake zachikunja. Kotero chizindikiro Cha pa thupi Cha kwa okhulupirira sichidangopatsidwa kokha ndi Ambuye wathu pa kulengedwa kwathu ayi koma kwatsimikiziridwa mu kuuka kwake.

    Tsopano atauka adakwera kumwamba komwe ali ku dzanka la manga la Atate, Ambuye Yesu Khristu ali moyo kwa Atate kutipempherera ife monga wansembe wamkulu. Kudzera mu mawu ake ndi Mzimu wake iye amatiphunzitsa kupemphera pokhala iye ndiye mkhalapakati wathu ndi otipembedzera kumwamba kwa Atate, Iye amayeretsa mapemohero athu ndi kuwapeleka kwa Atate mu dzina lake. Ndipo tsiku lina (angakhale palibe adziwa za tskulo kapena nthawi koma Atate yekha) adzabwereranso muulemerero wake monga momwe adakwerera kumwamba, kudzalamulira dziko lapansi, kudzadzutsa akufa kukonzekera chiweruzo ndi kukhala pamodzi ndi anthu mu ulemelero wake.

    Pakubweranso kwake ngati Mfumu, Khristu Mulungu wathu adzathetsa kuphinjika konse ndi chisalungamo pa dziko lapansi. Koma tsopano pamene tidikira, Iye akulamura ngati Mfumu ya mafuko onse komanso kutipulumutsa ife ndipo adzachotsa kuphinjika konse ndi chisalungamo. Ngati tidikira mwachidwi za kubweranso kwake kudzalamulira ndipo tidzapemphera kuti ‘Ufumu wanu sitidzakana chigonjetso chake Cha pa moyo wathu pamene watenga ulamuliro pa moyo wathu ngati zake komanso adani athu (kuphatikizapo machimo). M'malo mwake pamene tifunafuna Ufumu wake ndi kubwereranso kwake kwa iye amene apukuta misonzi yathu yonse ndi kuthetsa masauko athu onse ndi kupweteka kwantundu wina ulionse, tiyenera kukhala mchiyenbekezo Cha Ufumu wake uli mkudza, pamene tikusakasaka (mukulumikizana ndi iye) kuti atichotsere misonzi yathu ndi kutonthoza iwo akulira, kuvutika pamodzi ndi iwo akuvutika, kupanga mabala a iwo oponderezedwa ndipo ali mu ululu. Lamulo la Mfumu yathu ndi lakuti’ tisenzerane zothodwetsa wina ndi nzakendi kukwaniritsa lamulo la Khristu (Agalatiya 6:2) monga achitira mpulumutsi wathu, tidzipeleka tokha kwa wina ndi nzake nsembe ya chikondi. (Zekaria 14:4; Mateyu 1:23; 24:30; 28:5-6; Luka 1:35; Yohane 14:30,20:3-18; Machitidwe 1:9,11; Aroma1:4; 5:11; 2Akorinto 5:29-21; Afilipi 2:6-11; 1Atesalonika 4:15-17; 1 Timoteo 3:16; Ahebri 2:17,4:15,7:25-26; 1 Yohane 2:1-2; Chibvumbulutso 1:7; 20:1-15)

  • Chipulumutso Cha dziko- Cha anthu a mtundubwina ulionse ndi malankhulidwe osiyanasiyana- zikubwera kudzera mwa ntchito imene Khristu adaitsiriza. Pali chipulumutso chimodzi chimene tikuitanidwira kuti tikagawane kudzera mwa mpulumutsi m’modzi amene adadzipeleka yekha m’mako mwathu. Ubale umene tili nawo mwa Khristu Yesu ndi ntchito ya Mzimu Woyera kudzera mu chikhulupiriro chimene chidabwera titamva mawu a uthenga wabwino. Talimikizanitsidwa kwa Yesu Khristu ndipo okhulupirira amapeza mwa iye chisomo chochuluka Cha kulungamitsidwa ndi kuyeretsedwa.

     Muchisomo chake iye adzalungamitsa iwo amene apumira ndi kudalira mwa Yesu Khristu mu chikhulupiriro, Ambuye Mulungu amatikhululukira machimo athu ndi kutilandira ngati oyera pamaso pake kudzera mu chiyero Cha Khristu yekha basi (mu moyo wake opanda uchimo ndi imfa yolipira machimo athu pa mtanda) zidaikidwa pa ife. Kudzera mu mphatso ya chisomoyi, onse amene akhulupirira avalikidwa chiyero Cha Khristu mwa chisomo chokha, kudzera muchikhulupiriro chokha. Komabe, kuvomereza Mwana okondedwa wa Mulunguyi kumene okhulupirira onse amagawana sikutanthauza kusinthika kwenikweni. Kuvalikidwa chovala Cha chiyero sizochoka kwa ife ayi, ifeyo tili mbali zonse ziwiri achiyero komanso auchimo. Tchimo m’moyo mwathu silimangichoka wamba, koma limayenera kuti lizindikiridwe, ndi kuvomerezedwa ndi kulapidwa. Choonadi Cha uchimo pa moyo wathu chikuyenera chisakanidwe kapena kubisidwa, lemba likuti ‘ngati tinena kuti tilibe uchimo tidzinyenga tokha ndipo choonadi sichili mwa ife (1 John 1:8;10); koma ngati wina achimwa tili naye otilankhulira kwa Atate, Yesu Khristu woyerayo. Iye yekhayo ndiye amene ali dipo la machimo athu popeza adalipira kale pa mtanda. (1 John 2:1-2)

    Iwo amene adabadwa mwatsopano Ali mwa Khristu ovekedwa chiyero chake ndi kulengedwa ana ake a amuna ndi a akazi a Mulungu wa moyo. Ndipo timalandira chiyeretso nthawi zonse mwa Mulungu wathu ndi cholinga choti tithe kufanana naye Yesu Khristu mu chiyero. Chiyeretso ndi kusinthika ku chimene ife tili mkukhala olengedwa watsopano mwa Khristu izi sizitanthauza kuti zifufuta chikhalidwe chathu ngati olengedwa ayi. Kudzera mu chisomo chakutiyeretsachi timasandulika pang’ono ndi pang’ono kukhala muchifanizo Cha Mulungu popeza tidalengedwa muchifanizo chake ndipo tikubwezeretsedwa kuchifanizo chakecho.

    Monga Mzimu Woyera amene akhalita mwa ife amatiyeretsa mwa mawu a Mulungu, taitanidwa kuti tikalikane tchimo tsiku ndi tsiku kudzera mu chisomo Cha Mulungu- pakupha zintchito za uchimo ndi zikhumbitso zake- ndikukhala ku chiyero, kukura mu chisomo ndi chiyero chenicheni pa kuopa Mulungu. Izi timachita podalira mapembedzero a Khristu kwa ife ndi mu mphamvu ya Mzimu wa chisomo, ndi chitsimikizo ‘kuti iye amene waiyamba ntchito yabwino mwa ife adzaimalizitsa kufikira tsiku lakubwera Khristu Yesu’ (Filimoni 1:6) (Aroma 3:24; 5:1-9; 6:6, 11-14, 8:33, 10:4; 1Akorinto 6:11; 2 Akorinto 7:1; Ahebri 10:10).

  • Kuchokera kuwamba, Ambuye Yesu Khristu amene adakwera kumwamba amatsanulira lonjezo la Atate la Mzimu Woyera pa anthu ake. Mzimu Woyera amakhala mwa okhulupirira onse, popeza ndi iye Mzimuyo amene amatsutsa tchimo m’moyo mwathu ndi kutikokera ku chipulumutso Cha Khristu kutiombanso ndi kutilumikizitsa kwa Khristu mwa chikhulupiriro.

    Pamene Khristu atibatiza mwa Mzimu Woyera, timalandira Mzimu Woyera mwa njira yotsanulira chikondi Cha Mulungu pa mtima wathu kutitsimikizira kuti ndife ana ake ndi kutipatsa ife mphamvu ya kutumikira iye ndi kulalikira kwa ena za uthenga wabwino wa chipulumutso mwa Yesu. Mpulumutsi wathu akutiphunzitsa kuti tidzipemphera kuti tilandire Mzimu Woyera ngati mphatso ya bwino.

    Ubatizo uwu wa Mzimu Woyera walonjezedwa kwa wina aliyense ‘lonjezo ili Lili kwa inu ndi ana anu ndi kwa iwo amene ali kutali, anthu ochiluka amene ambuye Mulungu angawaitane’ Machitidwe 2:39). Izi zikuonetsera za moyo uli mkudza umene tidzaulandire osiyana ndi kubadwanso, wotsatiridwa ndi zozizwa kuchokera pa chiyambi. (Luka 3:16; 11:9-13; 24:29; Yohane 7:37-39; Machitidwe 1: 4-5; 2:1-4,38-39; 10:46; 19:6; Aefeso 5:18)

  • Mpingo umene ndi thupi la Khristu ndi umodzi, Woyera, waponse ponse ndi wa utumwi. Pali thupi limodzi lolumikizidwa ku mutu umodzi ndiye Yesu Khristu komwe moyo ndi chidzalo zimafumira. Khristu adabwera padziko lapansi kamodzi nadzipeleka yekha pamtanda kamodzi ndipo adauka, nakwera kumwamba ku dzanja la manja la Atate kamodzi, popeza ndi thupi limodzi limene walilimikizanitsa kwa iye mwini. Sipangakhale kugawikana kuthupi la Khristu popeza ndife tonse amodzi mwa Khristu. Padziko lapansi mpingo imadziwika kuti ndi kumene choonadi ndi chikhulupiriro, komwe mawu a Mulungu amalalikidwa, kumene miyambo ya mtchalitchi imachitika, kumene nkhosa zimasamalidwa, kutetezedwa ndi kudyetsedwa ndi oweta nkhosa okhulupirika kudzera mu kuphunzitsa ndi mwambo.

    Thupi limodzili limatchulidwa loyera mwa Khristu ndipo limasinthika pang’ono pang’ono kumafanana ndi Yesu mchiyero ndipo liyenera kumatsukidwa uchimo ndi kukura kufikira muchikondi choyera, ‘mu kachisi wake Woyera…. momwe Mulungu agonera mwa Mzimu’ (Aefeso 2:22). Mpingo woyerawu ndi wa ponseponse- thupi limene lakuta dziko lonse, zilankhuro zonse, zikhalidwe zonse, mitundu yonse, anthu a zaka zosiyana siyana komanso opeza mosiyana lemba likuti pa Akolosw 3:11 ‘Pamene palibe Mgriki kapena myuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Msukuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m’zonse.

    Tonse tidagulidwa ndi mwazi wa Yesu ndipo tayanjanitsidwa ndi Mzimu mmodzi ku mutu umodzi muthupi limodzi. Umodzi wa thupi la Khristu ukuonekera pa kulalikira kwa mpingo ponseponse. Ndipo uwu, ndi oyera, mpingo wa ponse ponse ndi wa utumwi: omwe ndi wa mitundu yosiyana siyana ndi ziyankhuro zosiyana siyana lomwe lakuta dziko la pansi kulaklikira uthenga wabwino umene udapelekedwa kwa Atumwi oyamba kotero pamene tilalikira Yesu Khristu ku mitundu yosiyana siyana ndi ziyankhuro zosiyana siyana kuwaitanira kwa Khristu kuti alandire chipulumutso ndi moyo ndi kuonjezeredwa ku mpingo wake.

    Potsanulira Mzimu wake ku mpingo Khristu amalandira ulemelero ndipo mpingo umamangika, kulimbikitsika ndipo umalandira chitonthozo kupyolera mu mphatso ya mawu a nzeru, mawu a chidziwitso, chikhulupiriro, mphatso ya machiritso, zozizwa, uneneri, kuzindikira mizimu, malilime osiyanasiyana ndi kumasulira malilime. Ambuye Yesu akutilimbikitsa kuti tikhumbe kukhala ndi mphatso zimenezi zimene Mulungu amagawa malinga ndi akufuna kwake kuti zikapindukire mpingo. Izi ndi mphatso zochokera mchisomo Cha Mulungu, sizilandiridwa kamba ka mwayinwa munthu kotero ziyenera zitisogolere ku kudzichepetsa, odzala ndi chithokozo ndi kudalira pa chisomo Cha Mulungu ndipo mphatsozi zigwiritsidwe ntchito muchikhulupiriro ndi chikondi.

    (1 Akorinto 12:4-11; 14:3; 12, 26; Aefeso 1: 23; 4:12)

  • Ambuye wathu Yesu Khristu adapeleka ku mpingo wake zizindikiro za utumiki monga: zinsisi ziwiri za zinthu, zimene adadzidalitsa ndi mawu ake omwe adatilonjeza kukakumana naye mu chisomo chake. Mu madzi a ubatizo timalumikizana ndi Khristu mu ubatizo uwiri, wa pa Yorodano ndi pa mtanda. Pamene okhulupirira abatizidwa m’madzi mudzina la Atate, la Mwana ndi la Mzimu Woyera Mulungu amalankhura uthenga wachikhululukiro Cha uchimo kudzera muubale wathu ndi Yesu Khristu mu imfa yake, kuikidwa m’manda ndi kuuka kwa akufa. Madzi a ubatizo amatilumikizanitsa ngati banja limodzi mwa Khristu ndipo akupitiliza kutiitanira kuti tikadye ndi kumwa pamodzi ndi anthu ake a ambuye pa gome la ambuye wathu.

    Pakunyema mkate, tichite izi mwa mantha ndi kudzichepetsa ndi chiyamiko. Timadya mkate umene Khristu mwini amautcha thupi lake ndi chikho chimene Khristu mwini amautcha mwazi wake, timakhala ndi thanzi ndi mpulumutsi wathu ndipo timalalikira za imfa yake kufikira atadzanso.

    Malemba akutiphunzitsa kuti tikuyenera kudziyesa tokha pamene tikhala tikubwera ku gome la ambuye pamene tikumbukira za mpulumutsi wathu ndipo timadya ndi chikhulupiriro oakuzindikira thupi la ambuye Yesu. Pakugawana mkate ndi chikho pa mgonero wa ambuye timakhala tikulandira mbuye wathu m’modzi yemweyo ndipo timakhala mu umodzi wa Thupi Lake. Mu chizindikiro Cha ubatizo ichi ambuye mwa Mzimu amatenga mkate ndi vinyo ndi kudzidalitsakoteto kudzera mu mgonerowu tikathe kukakumana naye muthupi ndi mwazi ku chiyeretso ndi chisamaliriro. Kukonzedwanso watsopano pa gome lake kumene imfa yake imalengezedwa, iye watituma kukalalikira za imfa yake kwa ena kuti nawonso akathe kulumikizidwa kwa Khristu kudzera mu kukhulupirira ndikubwera ku phwando lake la chisomo. (Mateyu 28: 19; Marko16:16; Luka 22:19-20; Machitidwe 2:38; 8:12, 36-38 Aroma 6:3-7; 1 Akorinto 10:15-21, 11:23-32)

  • Liwu la m’malembo oyera ndi liwu la Mulungu. Baibulo lonse ndi mawu owuzilidwa mpweya ndi Mulungu ndipo ali oona, Ali ndi ulamuliro omaliza ndipo ndiokwanira kuthandiza munthu kotheratu. Mabuku makumi asanu ndi mmodzi kudza mphambu zisanu m’chimodzi (66) a mchipangano chakale ndi mchipangano chatsopano mumbali zonse ndiouzilidwa mpweya ndi Mzimu Woyera kudzera mwa alembi osiyanasiyana amene adalemba mu chihelene (Greek, chiheberi ndi chiaramaiki) kotero nusu lina lililonse la malembo, tikunena kuti malembo onse ndi mawu ake enieni a Mulungu Monga mawu a Mulungu, mawuwa ali ndi ulamuliro wa Mulungu. Pokhala kuti ndi mawu a Mulungu alibe cholakwika. Mawu olembedwa a Mulungu amalalikira za Yesu Khristu amene ali mawu a Mulungu amoyo.

     Malembo Ali ndi zinthu zonse ziyenera pa chipulumutso Cha munthu komanso umulungu ndipo ndi okwanira kulondolera ku chikhulupiriro komanso pa chipembedzo. Palibe angasinthe mawu a Mulungu, angakhale chikhalidwe sichingasinthe mawu a Mulungu, angakhale lamulo la mfumu, masomphenya, kaya chozizwa kaya mavumbulutso amitundu wanji sangathe kuchotsera kapena kuonjezera. Baibulo likuyenera kukhulupiridwa ngati malangizo a Mulungu minjira zonse. Tiyeni tiwamvere ngati malamuko a Mulungu Monga chitsimikuzo cha malonjezano ake. Pamene malembo oyera alankhura, cholankhulidwacho chimakhala kuti chatheka. Pamene malembo alankhura, Mulungu wamoyo walankhura.

     Mulungu yemweyo amene wauzira mpweya malemba, amene wadziulura yekha m’malembo oyera, watitsekura maso athu kutitione kudabwitsa kwake m’mawu ake.  Pa kuunikilidwa ndi Mzimu Woyera ndi kudalira pa iye pamenepo amatithandizira kumvetsetsa mawu. Popeza iye amagwiritsa ntchito malemba ake kuti akalongosole malembo ake.

     Mawu a Mulungu ndi amphamvu komanso a moyo ndipo mwa mawu ake amapeleka moyo watsopano, chikhulupiriro, chiyeretso ndi kukura mu chisomo. Kudzera m’malembo ake amatikonzekeretsa ku ntchito yake ya bwino. Mawu ake ndi chida chimene chimabweretsa zipatso mumoyo wa iwo amene alingalira pa mawu ake. Ambuye Mulungu amagwira ntchito mwamphamvu ndi mawu ake ndipo mawu ake sabwerera kwa iye osapindura kanthu. Pamene tilalikira uthenga wa Mulungu mokhulupirika, Mulungu adzagwiritsa ntchito mawu ake kupangitsa ambiri ‘kuzindikira chipulumutso kudzera mu chikhulupiriro chimene chili mwa Khristu Yesu’ (2 Timoteyo 3:15; 2 Timoteyo 3:16; 2 Petro 1:21)

  • Monga mutu wa mpingo, ambuye Yesu amalamulira, amalondilera, amebweretsa umodzi, amapangitsa munthu kukhwima mu uzimu ndi kukuza thupi kukhala mtumwi oona, Mneneri oona, Mlaliki oona, Mbusa oona, mkulu wampingo ndi mphunzitsi oona. Ndipo mu zisomo zake amapeleka mphatso kwa Atumwi, Aneneri, Alaliki, Abusa (akulu ampingo) ndi aphunzitsi ku thupi lake la Khristu. Mautumiki amenewa saitanidwa paokha ayi koma kuchokera kwa Khristu Yesu pamene tidalira iye ndi kukhazikika mwa iye. Kukhazikika mu utumiki wa MPINGO wake wa Khristu ndiko kuti atumiki ake amakhala pansi ndi kumva mawu a Khristu modzichepetsa ndi muchikondi. Khristu amaonetsera mphamvu ya kumanga ndi kumasulira kudzera mwa atumiki ake pamene alalikira mawu ndi kupeleka mwambo mu mpingo.

     Atumiki, odzala ndi Mzimu Woyera ayitanidwa kukatumikira monga thupi limodzi la Khristu mu mpingo, pamodzi ndi atsogoleri ena onse. Uwu ndi utumiki wa uzimu, omwe umafuna kudzadzidwa ndi Mzimu Woyera, chithandizo, nzeru ndi kukhazikika mu pemphero. Mulungu amapatura amene wamusankha kuutumiki kudzera mukudzodza mwa pemphero ndi kusanjika manja kwa Atumwi ndi kupeleka chifundo Cha Mulungu. (Machitidwe 6:2-3,6; 13:1-3; 20:28;              2 Akorinto 11:28;Aefeso 4: 8-16; 1 Timoteyo 13; Tito 1:5-9; Ahebri 13:17 1Petro 5:1-4)

  • Yesu Khristu mwini ndiye chisomo Cha Mulungu Cha kupulumutsa, chimene timagawana naye mchikhulupiriro. Sitingathe kufunsa za kuthekera kumene Mulungu adakuika mwa Yesu Khristu kuti akapulumutse, kukasunga ndi kupangitsa okhulupirira wina aliyenae kuti akalandire chidzalo Cha ulemelero. Malemba akutifinsa kupilira pa chikhulupiriro chathu ca pa Khristu mpaka kumapeto kwa nthawi.

    Pamene Paulo amachenjeza za kugwa pamaso pa Mulungu, chenjezoli limapita kwa anthu amene uadaonjezera kanthu kena pamwamba pa kudalira Ambuye wathu Yesu Khristu ngati mpulumutsi (Agalatiya 5:4)

    Kusiya njira ya Khristu ndi kumukana iye zikutanthauza kukana chisomo Cha Mulungu Cha kupulumutsa. Amene adalira pa Khristu Ali otetezeka mwa iye. (Aroma11:20-22; Akolose 11:28; Ahebri 6:4-6; 10:26-29; 38-39; 2Petro2:20-22; CYnbvumulutso 22: 19)

  • Chikondi Cha Mulungu chimatisogolera kumukonda iye posunga malamuko ake (Yohane 14:15). Lamulo la Mulungu silidathetsedwe komatu Khristu akutiitana kuti tiwamvere malamulo ake monga chinthu chikoma poonetsa chikondi chathu pa mpulumutsi wathu. Zina mwa zomwe zimaonetsera chikondi chathu pa iye ndiko kukhulupirika pa chakhumi ndi chopeleka kuthandizira chosowa Cha mpingo monga mbali imodzi ya kupembedza, osati kuchita kukakamizidwa koma monga momwe mtima wafunira ndi mosangalala. Apa sitikungoyenera kupeleka kokha chakhumi ndi zopeleka kuiwala kusata malamulo a Mulungu: chilungamo, chisomo ndi chikhulupiriro (Mateyu 23:23). Monga momwe ambuye wathu wakhala akuuza anthu ake kuti adzikonda nzawo monga adzikondera iwo eni, Khristu mwini akupeleka lamulo lakuti’ mudzikondana wina ndi nzake’ (Yohane 13:34). Iye akupitiliza kunena kuti tilorere kutaya moyo wathu kamba ka nzathu yomwe ndi nsembe ya kwa ife. Ntchito zabwinonza kumvera ndi chikondi sizingatilungamitse,’ lemba linena kuti ntchito za chilamulo sizingatilungamitse (Agalatiya 2:16). Kwa iwo amene alungamitsidwa mwa chikhulupiriro Cha pa Yesu Khristu ndipo alumikizana ndi iye, ntchito zabwino zidzatumphuka kuchokera mu chikhulupiriro ngati chipatso.  Popanda Yesu palibe chomwe tingapange, koma iwo amene akhazikika mwa Yesu Khristu mwa chikhulupiriro adzabereka zipatso zochuluka mwa Mzimu Woyera zomwe zidzapeleke ulemelero kwa Mulungu. (Genesis 14:20, 28:22; Miyambo 3.9-10; Malaki 3:10; 1 Akorinto 16:2; 2 Akorinto 9:6-7; Ahebri 7:1-10)

Privacy Policy
Cookie Policy
Contact Us

Instagram

Facebook
Twitter

ACUK, Suite 110 Crystal House
New Bedford Road
Luton
LU1 1HS
United Kingdom


Theological training for Spirit-empowered ministry & mission.

Part of the Apostolic Church UK. Registered as a charity in England and Wales 284789 and Scotland SC037835.